Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 10:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndipo salandira inu, m'mene mwaturuka ku makwalala ace nenani,

11. Lingakhale pfumbi locokera kumudzi kwanu, lomamatika ku mapaziathu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ici, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.

12. Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodoma kudzapiririka kuposa mudzi umenewo.

13. Tsoka iwe, Korazini! tsoka iwe Betsaida! cifukwa kuti zikadacitika m'Turo ndi Sidoni zamphamvuzi zidacitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi obvala ciguduli ndi phulusa.

14. Koma ku Turo ndi Sidoni kudzapiririka m'ciweruziro, koposa inu.

15. Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku Hade,

16. iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana iye amene anandituma Ine.

17. Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.

18. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wocokera kumwamba.

Werengani mutu wathunthu Luka 10