Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:72-78 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

72. 16 Kucitira atate athu cifundo, Ndi kukumbukila pangano lace lopatulika;

73. Cilumbiro cimene iye anacilumbira kwa Abrahamu atate wathu,

74. Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu,17 Tidzamtumikira iye, opanda mantha,

75. 18 M'ciyero ndi cilungamo pamaso pace, masiku athu onse.

76. 19 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu:20 Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace;

77. Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso,21 Ndi makhululukidwe a macimoao,

78. Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;

Werengani mutu wathunthu Luka 1