Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:69-80 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

69. Ndipo iye anatikwezera ife nyanga ya cipulumutso,Mwa pfuko la Davine mwana wace,

70. 15 (Monga iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ace oyera mtima, a kale lomwe),

71. Cipulumutso ca adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife;

72. 16 Kucitira atate athu cifundo, Ndi kukumbukila pangano lace lopatulika;

73. Cilumbiro cimene iye anacilumbira kwa Abrahamu atate wathu,

74. Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu,17 Tidzamtumikira iye, opanda mantha,

75. 18 M'ciyero ndi cilungamo pamaso pace, masiku athu onse.

76. 19 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu:20 Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace;

77. Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso,21 Ndi makhululukidwe a macimoao,

78. Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;

79. 22 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa;Kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

80. Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wace, ndipo 23 iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Luka 1