Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:64-78 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

64. Ndipo 12 pomwepo panatseguka pakamwa pace, ndi lilume lace linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.

65. Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko: lonse la mapiri a Yudeya,

66. Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nangamwana uyu adzakhala wotani? Pakuti 13 dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.

67. Ndipo atate wace Zakariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,

68. Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israyeli;14 Cifukwa iye anayang'ana, nacitira anthu ace ciombolo,

69. Ndipo iye anatikwezera ife nyanga ya cipulumutso,Mwa pfuko la Davine mwana wace,

70. 15 (Monga iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ace oyera mtima, a kale lomwe),

71. Cipulumutso ca adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife;

72. 16 Kucitira atate athu cifundo, Ndi kukumbukila pangano lace lopatulika;

73. Cilumbiro cimene iye anacilumbira kwa Abrahamu atate wathu,

74. Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu,17 Tidzamtumikira iye, opanda mantha,

75. 18 M'ciyero ndi cilungamo pamaso pace, masiku athu onse.

76. 19 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu:20 Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace;

77. Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso,21 Ndi makhululukidwe a macimoao,

78. Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;

Werengani mutu wathunthu Luka 1