Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:51-62 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

51. Iye anacita zamphamvu ndi mkono wace;6 Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao,

52. iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yacifumu,Ndipo anakweza aumphawi,

53. 7 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino,Ndipo eni cuma anawacotsa opanda kanthu.

54. Anathangatira Israyeli mnyamata wace,Kuti akakumbukile cifundo,

55. 8 (Monga analankhula kwa makolo athu)Kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace ku nthawi yonse.

56. Ndipo Mariya anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwace.

57. Ndipo inakwanira nthawi ya Elisabeti, ya kubala kwace, ndipo anabala mwana wamwamuna.

58. Ndipo anansi ace ndi abale ace anamva kuti Ambuye anakulitsa cifundo cace pa iye; 9 nakondwera naye pamodzi.

59. Ndipo panali 10 tsiku lacisanu ndi citatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amuche dzina la atate wace Zakariya.

60. Ndipo amace anayankha, kuti, lai; koma 11 adzachedwa Yohane.

61. Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene achedwa dzina ili.

62. Ndipo anakodola atate wace, afuna amuche dzina liti?

Werengani mutu wathunthu Luka 1