43. Ndipo ici cicokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amace wa Ambuye wanga?
44. Pakuti ona, pamene mau a kulankhula kwako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.
45. Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; cifukwa zidzacitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.
46. 3 Ndipo Mariya anati,Moyo wanga ulemekeza Ambuye,
47. Ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.
48. Cifukwa iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wace;Pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzandichula ine wodala.
49. Cifukwa iye Wamphamvuyo anandicitira ine zazikuru;4 Ndipo dzina lace liri loyera.
50. 5 Ndipo cifundo cace cifikira anthu a mibadwo mibadwoPa iwo amene amuopa iye.
51. Iye anacita zamphamvu ndi mkono wace;6 Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao,
52. iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yacifumu,Ndipo anakweza aumphawi,
53. 7 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino,Ndipo eni cuma anawacotsa opanda kanthu.
54. Anathangatira Israyeli mnyamata wace,Kuti akakumbukile cifundo,