Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:33-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. ndipo iye adzacita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wace sudzatha.

34. Koma Mariya anati kwa mngelo, ici cidzacitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?

35. Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.

36. Ndipo taona, Elisabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wace; ndipo mwezi uno uli wacisanu ndi cimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

37. Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

38. Ndipo Mariya anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anacoka kwa iye.

39. Ndipo Mariya ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi cangu ku dziko la mapiri ku mudzi wa Yuda;

40. nalowa m'nyumba ya Zakariya, nalankhula Elisabeti.

41. Ndipo panali pamene Elisabeti anamva kulankhula kwace kwa Mariya, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwace; ndipo Elisabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;

42. nakweza mau ndi mpfuu waukuru, nati, 2 Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo codalitsika cipatso ca mimba yako,

43. Ndipo ici cicokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amace wa Ambuye wanga?

44. Pakuti ona, pamene mau a kulankhula kwako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.

45. Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; cifukwa zidzacitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.

46. 3 Ndipo Mariya anati,Moyo wanga ulemekeza Ambuye,

47. Ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

48. Cifukwa iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wace;Pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzandichula ine wodala.

49. Cifukwa iye Wamphamvuyo anandicitira ine zazikuru;4 Ndipo dzina lace liri loyera.

50. 5 Ndipo cifundo cace cifikira anthu a mibadwo mibadwoPa iwo amene amuopa iye.

51. Iye anacita zamphamvu ndi mkono wace;6 Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao,

52. iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yacifumu,Ndipo anakweza aumphawi,

Werengani mutu wathunthu Luka 1