Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:24-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo atatha masiku awa, Elisabeti mkazi wace anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,

25. Ambuye wandicitira cotero m'masiku omwe iye anandipenyera, kucotsa manyazi anga pakati pa anthu.

26. Ndipo mwezi wacisanu ndi cimodzi mngelo Gabrieli anatumidwa ndi Mulungu kunka ku mudzi wa ku Galileya dzina lace N azarete,

27. kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lace Yosefe, wa pfuko la Davine; ndipo dzina lace la namwaliyo ndilo Mariya.

28. Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wocitidwa cisomo, Ambuye ali ndi iwe.

29. Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulankhula uku nkutani.

30. Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Mariya; pakuti wapeza cisomo ndi Mulungu.

31. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamucha dzina lace Yesu.

32. Iye adzakhala wamkuru, nadzachedwa Mwana wa Wamkurukuru: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wacifumu wa Davine atate wace:

33. ndipo iye adzacita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wace sudzatha.

34. Koma Mariya anati kwa mngelo, ici cidzacitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?

35. Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.

36. Ndipo taona, Elisabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wace; ndipo mwezi uno uli wacisanu ndi cimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

37. Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

Werengani mutu wathunthu Luka 1