Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Filemoni 1:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;

6. kuti ciyanjano ca cikhulupiriro cako cikakhale camphamvu podziwa cabwino ciri conse ciri mwa inu, ca kwa Kristu.

7. Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.

8. Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,

9. koma makamaka ndidandaulira mwa cikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Kristu Yesu;

10. ndikudandaulira cifukwa ca mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo,

11. amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;

12. amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weni weni wa ine.

13. Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino:

14. koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kucita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.

15. Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi cifukwa ca ici, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse;

16. osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.

17. Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.

18. Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;

Werengani mutu wathunthu Filemoni 1