Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Filemoni 1:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukila iwe m'mapemphero anga,

5. pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;

6. kuti ciyanjano ca cikhulupiriro cako cikakhale camphamvu podziwa cabwino ciri conse ciri mwa inu, ca kwa Kristu.

7. Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.

8. Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,

9. koma makamaka ndidandaulira mwa cikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Kristu Yesu;

10. ndikudandaulira cifukwa ca mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo,

11. amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;

Werengani mutu wathunthu Filemoni 1