Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Filemoni 1:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kucita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.

15. Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi cifukwa ca ici, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse;

16. osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.

17. Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.

18. Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;

19. Ine Paulo ndicilemba ndi dzanja langa, ndidzacibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.

20. Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Kristu.

21. Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzacicanso koposa cimene ndinena.

22. Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.

23. Epafra wandende mnzanga mwa Kristu Yesu akulankhula iwe;

24. ateronso, Marko, Aristarko, Dema, Luka, anchito anzanga.

25. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen.

Werengani mutu wathunthu Filemoni 1