Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Filemoni 1:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, wandende wa Kristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wanchito mnzathu,

2. ndi kwa Apiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikari mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako;

3. Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.

4. Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukila iwe m'mapemphero anga,

5. pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;

6. kuti ciyanjano ca cikhulupiriro cako cikakhale camphamvu podziwa cabwino ciri conse ciri mwa inu, ca kwa Kristu.

7. Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.

8. Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,

Werengani mutu wathunthu Filemoni 1