Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 3:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sarde lemba:Izi anena iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi riwiri: Ndidziwa nchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.

2. Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira, zimene zinafuna kufa; pakutisindinapeza nchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga.

3. Cifukwa cace kumbukila umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yace ndidzadza pa iwe.

4. Komatu uli nao maina owerengeka m'Sarde, amene sanadetsa zobvala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; cifukwa ali oyenera.

5. Iye amene alakika adzambveka motero zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lace m'buku la moyo, ndipo ndidzambvomereza dzina lace pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ace.

6. Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 3