Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 11:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto uturuka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ace ayenera kutero.

6. Izo ziti nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a cinenero cao; ndipo ulamuliro ziti nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi iri yonse zikafuna.

7. Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao cirombo eokwera kuturuka m'phompho cidzacita nazo nkhondo, nicidzazilaka, nicidzazipha izo.

8. Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala la mudzi waukuru, umene uchedwa, ponena zacizimu, Sodoma ndi Aigupto, pameneponso Ambuye wao anapacikidwa.

9. Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lace, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 11