Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 11:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipoanandipatsa ine bango ngati ndodo, ndikuti, Tanyamuka, nuyese Kacisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.

2. Ndipo bwalo la kunja kwa Kacisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.

3. Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zobvala ciguduli.

4. Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikapo nyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.

5. Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto uturuka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ace ayenera kutero.

6. Izo ziti nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a cinenero cao; ndipo ulamuliro ziti nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi iri yonse zikafuna.

7. Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao cirombo eokwera kuturuka m'phompho cidzacita nazo nkhondo, nicidzazilaka, nicidzazipha izo.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 11