Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 1:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira iye. Terotu. Amen.

8. Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

9. Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'cisautso ndi ufumu ndi cipiriro zokhala m'Yesu, ndinakhala pa cisumbu cochedwa Patmo, cifukwa ca mao a Mulungu ndi umboni wa Yesu.

10. Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akuru, ngati a lipenga,

11. ndi kuti, Cimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.

12. Ndipo ndinaceuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditaceuka ndinaona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi;

13. ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa munthu atabvala cobvala cofikira ku mapazi ace, atamangira lamba lagolidi pacifuwa.

14. Ndipo tsitsi la pamutu pace linali loyera ngati ubweya woyera, ngati cipale cofewa; ndi maso ace ngati lawi la moto;

15. ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ace ngati mkokomo wa madzi ambiri.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 1