Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 9:7-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. kapena cifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isake, mbeu yako idzaitanidwa.

8. Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yace.

9. Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana

10. Ndipo si cotero cokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isake;

11. pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo,

12. cotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.

13. Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.

14. Ndipo tsono tidzatani? Kodi ciripo cosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.

15. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzacitira cifundo amene ndimcitira cifundo, ndipo ndidzakhala ndi cisoni kwa iye amene ndikhala naye cisoni.

16. Cotero sicifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene acitira cifundo.

17. Pakuti lembo linena kwa Farao, Cifukwa ca ici, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.

18. Cotero iye acitira cifundo amene iye afuna, ndipo amene iye afuna amuumitsamtima.

19. Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza cifuno cace?

20. Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi cinthu copangidwa cidzanena ndi amene anacipanga, U ndipangiranji ine cotero?

Werengani mutu wathunthu Aroma 9