Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 9:23-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. ndi kuti iye akadziwitse ulemerero wace waukuru pa zotengera zacifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero,

24. ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?

25. Monga atinso mwa Hoseya,Amene sanakhala anthu anga, ndidzawacha anthu anga;Ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.

26. 1 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai,Pomwepo iwo adzachedwa ana a Mulungu wamoyo.

27. Ndipo Yesaya apfuula za Israyeli, kuti,2 Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga mcenga wa kunyanja, 3 cotsalira ndico cidzapulumuka.

28. Pakuti Ambuye adzacita mau ace pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwacidule.

29. Ndipo monga Yesaya anati kale,4 Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu,Tikadakhala monga Sodoma, ndipo tikadafanana ndi Gomora.

30. Cifukwa cace tidzatani? 5 Kuti amitundu amene sanatsata cilungamo, anafikira cilungamo, ndico cilungamo ca cikhulupiriro;

31. 6 koma Israyeli, potsata lamulo la cilungamo, sanafikira lamulolo.

32. Cifukwa canji? Cifukwa kuti sanacitsata ndi cikhulupiriro, koma monga ngati ndi nchito. 7 Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;

33. monganso kwalembedwa, kuti,8 Onani, ndikhazika m'Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa;Ndipo 9 wakukhulupirira iye sadzacita manyazi.

Werengani mutu wathunthu Aroma 9