Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 9:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza cifuno cace?

20. Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi cinthu copangidwa cidzanena ndi amene anacipanga, U ndipangiranji ine cotero?

21. Kodi kapena woumba mbiya sakutha kucita zace padothi, kuumba ndi ncinci yomweyo cotengera cimodzi caulemu ndi cina camanyazi?

22. Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuonetsa mkwiyo wace, ndi kudziwitsa mph amvu yace, analekerera ndi cilekerero cambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera cionongeko?

23. ndi kuti iye akadziwitse ulemerero wace waukuru pa zotengera zacifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero,

24. ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?

Werengani mutu wathunthu Aroma 9