Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 9:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinena zoona mwa Kristu, sindinama ai, cikumbu mtima canga cicita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,

2. kuti ndagwidwa ndi cisoni cacikuru ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.

3. Pakuti ndikadafunakuti ine ndekha nditembereredwe kundicotsa kwa Kristu cifukwa ca abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;

4. ndiwo Aisrayeli; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m'kacisi wa Mulungu, ndi malonjezo;

5. a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anacokera Kristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka ku nthawi zonse. Amen.

6. Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala cabe ai. Pakuti onse akucokera kwa a Israyeli siali Israyeli;

7. kapena cifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isake, mbeu yako idzaitanidwa.

8. Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yace.

9. Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana

10. Ndipo si cotero cokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isake;

11. pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo,

12. cotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.

Werengani mutu wathunthu Aroma 9