Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 8:34-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. 9 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, 10 amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, 11 amenenso atipempherera ife.

35. Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?

36. Monganso kwalembedwa,12 Cifukwa ca Inu tirikuphedwa dzuwa lonse;Tinayesedwa monga nkhosa zakupha,

37. Koma 13 m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.

38. Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu,

39. ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 8