Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 5:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo si cotero cokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti cisautso cicita cipiriro; ndi cipiriro cicita cizolowezi;

4. ndi cizolowezi cicita ciyembekezo:

5. ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

6. Pakuti pamene tinali cikhalire ofok a, pa nyengo yace Kristu anawafera osapembedza.

7. Pakuti ndi cibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.

8. Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.

9. Ndipo tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.

10. Pakuti ngati, pokhala ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wace.

11. Ndipo si cotero cokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene talandira naye tsopano ciyanjanitso.

12. Cifukwa cace, monga ucimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa ucimo; cotero imfa inafikira anthu onse, cifukwa kuti onse anacimwa.

Werengani mutu wathunthu Aroma 5