Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 5:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu;

2. amene ife tikhoza kulowa naye ndi cikhulupiriro m'cisomo ici m'mene tirikuunamo; ndipo tikondwera m'ciyembekezo ca ulemerero wa Mulungu.

3. Ndipo si cotero cokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti cisautso cicita cipiriro; ndi cipiriro cicita cizolowezi;

4. ndi cizolowezi cicita ciyembekezo:

5. ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Werengani mutu wathunthu Aroma 5