Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 4:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo iye osafoka m'cikhulupiriro sanalabadira thupi lace, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;

20. ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka cifukwa ca kusakhulupirira, koma analimbika m'cikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,

21. nakhazikikanso mumtima kuti, o cimene iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakucicita.

22. Cifukwa cace ici cinawerengedwa kwa iye cilungamo.

23. Ndipo ici sicinalembedwa cifukwa caiye yekha yekha, kuti cidawerengedwa kwa iye;

24. koma cifukwa ca ifenso, kwa ife amene cidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu,

25. amene anaperekedwa cifukwa ca zolakwazathu, naukitsidwa cifukwa ca kutiyesa ife olungama.

Werengani mutu wathunthu Aroma 4