Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, analandira ciani?

2. Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama cifukwa ca nchito, iye akhala naco codzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai.

3. Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo cinawerengedwa kwa iye cilungamo,

4. Ndipo kwa iye amene agwira nchito, mphotho siiwerengedwa ya cisomo koma ya mangawa.

5. Koma kwa iye amene sacita, koma akhulupirira iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, cikhulupiriro cace ciwerengedwa cilungamo.

6. Monganso Davide anena za mdalitso wace wa munthu, amene Mulungu amwerengera cilungamo copanda nchito,

7. ndi kuti,Odala iwo amene akhululukidwa kusayeruzika kwao,Nakwiriridwa macimo ao,

8. Wodala munthu amene Mulungu samwerengera ucimo.

9. Mdalitso umenewu tsono uli kwa odulidwa kodi, kapena kwa osadulidwa omwe? pakuti timati, Cikhulupiriro cace cinawerengedwa kwa Abrahamu cilungamo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 4