Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 3:19-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo tidziwa kuti zinthu ziri zonse cizinena cilamulo cizilankhulira iwo ali naco cilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;

20. cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi Debito za lamulo; pakuti ucimo udziwika ndi lamulo.

21. Koma tsopano cilungamo ca Mulungu caoneka copanda lamulo, cilamulo ndi aneneri acitira ici umboni;

22. ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana;

23. pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

24. ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;

25. amene Mulungu anamuika poyera akhale cotetezera mwa cikhulupiriro ca m'mwazi wace, kuti aonetse cilungamo cace, popeza Mulungu m'kulekerera kwace analekerera macimo ocitidwa kale lomwe;

26. kuti aonetse cilungamo cace m'nyengo yatsopano; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu,

27. Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La nchito kodi? lai; koma ndi lamulo la cikhulupiriro.

28. Pakuti timuyesa munthu wohmgama cifukwa ca cikhulupiriro, wopanda nchito za lamulo.

29. Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okha okha kodi? si wao wa amitundunso kodi? Bya, wa amitundunso:

30. ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi cikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa cikhulupiriro,

31. Potero kodi lamulo tiyesa cabe mwa cikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 3