12. Onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pace;Palibe mmodzi wakucita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.
13. M'mero mwao muli manda apululu;Ndi lilime lao amanyenga; Ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;
14. M'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;
15. Miyendo yao icita liwiro kukhetsa mwazi;
16. Kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao;
17. Ndipo njira ya mtendere sanaidziwa;
18. Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.
19. Ndipo tidziwa kuti zinthu ziri zonse cizinena cilamulo cizilankhulira iwo ali naco cilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
20. cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi Debito za lamulo; pakuti ucimo udziwika ndi lamulo.
21. Koma tsopano cilungamo ca Mulungu caoneka copanda lamulo, cilamulo ndi aneneri acitira ici umboni;
22. ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana;
23. pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;
24. ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;
25. amene Mulungu anamuika poyera akhale cotetezera mwa cikhulupiriro ca m'mwazi wace, kuti aonetse cilungamo cace, popeza Mulungu m'kulekerera kwace analekerera macimo ocitidwa kale lomwe;
26. kuti aonetse cilungamo cace m'nyengo yatsopano; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu,