Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 2:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'cilamulo ndi cionekedwe ca nzeru ndi ca coonadi;

21. ndiwe tsono wakuphunzitsa wina; kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?

22. Iwe wakunena kuti munthu asacite cigololo, kodi umacita cigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'kacisi kodi?

23. Iwe wakudzitamandira pacilamulo, kodi ucitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'cilamulo?

24. Pakuti dzina la Mulungu licitidwa mwano cifukwa ca inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.

25. Pakuti inde mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umacita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa.

26. Cifukwa cace ngati wosadulidwa asunga zoikika za cilamulo, kodi kusadulidwa kwace sikudzayesedwa ngati mdulidwe?

27. Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa cibadwidwe, ngati kukwanira cilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?

28. Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo;

Werengani mutu wathunthu Aroma 2