Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 2:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu;

18. nudziwa cifuniro cace, nubvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'cilamulo,

19. nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,

20. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'cilamulo ndi cionekedwe ca nzeru ndi ca coonadi;

21. ndiwe tsono wakuphunzitsa wina; kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?

22. Iwe wakunena kuti munthu asacite cigololo, kodi umacita cigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'kacisi kodi?

23. Iwe wakudzitamandira pacilamulo, kodi ucitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'cilamulo?

24. Pakuti dzina la Mulungu licitidwa mwano cifukwa ca inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.

Werengani mutu wathunthu Aroma 2