Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 2:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. pakuti Mulungu alibe tsankhu.

12. Pakuti onse amene anacimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anacimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;

13. pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akucita lamulo adzayesedwa olungama,

14. Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amacita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;

15. popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;

16. tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Kristu zinsinsi za anthu, monga mwa uthenga wanga wabwino.

17. Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu;

18. nudziwa cifuniro cace, nubvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'cilamulo,

19. nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,

20. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'cilamulo ndi cionekedwe ca nzeru ndi ca coonadi;

21. ndiwe tsono wakuphunzitsa wina; kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?

Werengani mutu wathunthu Aroma 2