Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 2:1-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umacita zomwezo.

2. Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akucita zotere.

3. Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akucita zotere, ndipo uzicitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wit Mulungu?

4. Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wace, ndi cilekerero ndi cipiriro cace, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?

5. Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa dzuwa la mkwiyo ndi la kubvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;

6. amene adzabwezera munthu ali yense kolingana ndi nchito zace;

7. kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi cisaonongeko, mwa kupirira pa nchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;

8. koma kwa iwo andeu, ndi osamvera coonadi, koma amvera cosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,

9. nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu ali yense wakucita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mhelene;

10. koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu ali yense wakucita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene;

11. pakuti Mulungu alibe tsankhu.

12. Pakuti onse amene anacimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anacimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;

13. pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akucita lamulo adzayesedwa olungama,

14. Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amacita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;

15. popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;

16. tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Kristu zinsinsi za anthu, monga mwa uthenga wanga wabwino.

17. Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu;

18. nudziwa cifuniro cace, nubvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'cilamulo,

19. nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,

20. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'cilamulo ndi cionekedwe ca nzeru ndi ca coonadi;

21. ndiwe tsono wakuphunzitsa wina; kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?

Werengani mutu wathunthu Aroma 2