Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 16:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Mulankhule Ampliato wokondedwa wanga mwa Ambuye.

9. Mulankhule Urbano wanchito mnzathu mwa Kristu, ndi Staku wokondedwa wanga,

10. Mulankhule Apele, wobvomerezedwayo mwa Kristu, Mulankhule iwo a kwa Aristobulo.

11. Mulankhule Herodiona, mbale wanga. Mulankhule iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye.

12. Mulankhule Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa nchito mwa Ambuyeo Mulankhule. Persida, wokondedwayo amene anagwiritsa nchito zambiri mwa Ambuye.

13. Mulankhule Rufo, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wace ndi wanga.

14. Mulankhule Asunkrito, Felego, Herme, Patroba, Henna ndi abale amene ali nao.

15. Mulankhule Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wace, ndi Olumpa, ndi oyeramtima onse ali pamodzi nao.

16. Mulankhulane wina ndi mnzace ndi kupsompsona kopatulika. Mipingo yonse ya Kristu ikulankhulani inu.

17. Ndipo ndikudandaulirani; abale, yang'anirani iwo akucita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi ciphunzitsoco munaciphunzira inu; ndipopotolokani pa iwo.

18. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asoceretsamitiina ya osalakwa.

19. Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Cifukwa cace ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.

20. Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.

21. Timoteo wanchito mnzanga akulankhulani inu; ndi Lukiyo ndi Yasoni ndi Sosipatro, abale anga.

Werengani mutu wathunthu Aroma 16