Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 16:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. ndipo mulankhule Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Mulankhule Epeneto wokondedwa wanga, ndiye cipatso coundukula ca Asiya ca kwa Kristu,

6. Mulankhule Mariya amene anadzilemetsa ndi nchito zambiri zothandiza inu.

7. Mulankhule Androniko ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa amitumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Kristu.

8. Mulankhule Ampliato wokondedwa wanga mwa Ambuye.

9. Mulankhule Urbano wanchito mnzathu mwa Kristu, ndi Staku wokondedwa wanga,

10. Mulankhule Apele, wobvomerezedwayo mwa Kristu, Mulankhule iwo a kwa Aristobulo.

11. Mulankhule Herodiona, mbale wanga. Mulankhule iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye.

12. Mulankhule Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa nchito mwa Ambuyeo Mulankhule. Persida, wokondedwayo amene anagwiritsa nchito zambiri mwa Ambuye.

13. Mulankhule Rufo, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wace ndi wanga.

14. Mulankhule Asunkrito, Felego, Herme, Patroba, Henna ndi abale amene ali nao.

15. Mulankhule Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wace, ndi Olumpa, ndi oyeramtima onse ali pamodzi nao.

Werengani mutu wathunthu Aroma 16