Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 15:28-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Koma pamene ndikatsiriza ici, ndi kuwasindikizira iwo cipatso ici, ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.

29. Ndipo 4 ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwace kwa cidalitso ca Kristu.

30. Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;

31. kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;

32. 6 kuti ndi cimwemwe ndikadze kwa inu mwa cifuno ca Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.

33. Ndipo 7 Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.

Werengani mutu wathunthu Aroma 15