Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 15:20-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.

21. Koma monga kwalembedwa,Iwo amene uthenga wace sunawafikire, adzaona,Ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.

22. Cifukwa cacenso ndinaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu;

23. koma tsopano, pamene ndiribe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,

24. pamene pali ponse ndidzapita ku Spanya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.

25. Koma 1 tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndirikutumikira oyera mtima.

26. Pakuti 2 kunakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya kucereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.

27. Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. 3 Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikica iwo ndi zinthu zathupi.

28. Koma pamene ndikatsiriza ici, ndi kuwasindikizira iwo cipatso ici, ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.

29. Ndipo 4 ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwace kwa cidalitso ca Kristu.

30. Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;

31. kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;

32. 6 kuti ndi cimwemwe ndikadze kwa inu mwa cifuno ca Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 15