Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 15:18-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,

19. mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu;

20. ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.

21. Koma monga kwalembedwa,Iwo amene uthenga wace sunawafikire, adzaona,Ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.

22. Cifukwa cacenso ndinaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu;

23. koma tsopano, pamene ndiribe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,

24. pamene pali ponse ndidzapita ku Spanya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.

25. Koma 1 tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndirikutumikira oyera mtima.

26. Pakuti 2 kunakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya kucereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 15