Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 15:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, cifukwa ca cisomo capatsidwa kwa ine ndi Mulungu,

16. kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.

17. Cifukwa cace ndiri naco codzitamandira ca m'Kristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.

18. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,

19. mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu;

20. ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.

21. Koma monga kwalembedwa,Iwo amene uthenga wace sunawafikire, adzaona,Ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.

22. Cifukwa cacenso ndinaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu;

23. koma tsopano, pamene ndiribe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,

Werengani mutu wathunthu Aroma 15