Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 15:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofoka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.

2. Yense wa ife akondweretse mnzace, kumcitira zabwino, zakumlimbikitsa.

3. Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe Inagwa pa Ine,

4. Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.

5. Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;

6. kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.

7. Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.

8. Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,

9. ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa ca cifundo; monga kwalembedwa,Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu,Ndidzayimbira dzina lanu.

10. Ndiponso anena,Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.

Werengani mutu wathunthu Aroma 15