Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 14:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofoka angodya zitsamba.

3. Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.

4. Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wace? iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wace wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.

5. Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzace; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu ali yense akhazikike konse mumtima mwace.

6. Iye wakusamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu.

7. Pakuti palibe mmodzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha, ndipo palibe mmodzi adzifera yekha.

8. Pakuti tingakhale tiri ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; cifukwa cace tingakhale tiri ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ace a Ambuye.

9. Pakuti, cifukwa ca ici Kristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 14