Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 13:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wocokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.

2. Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza coikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga

3. Pakuti mafumu sakhala oopss nchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro: Cita cabwino, ndipo udzalandirs kutama m'menemo:

4. pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kucitira iwe zabwino. Koma ngati ucita coipa opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwacabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwe zera cilango wocita zoipa.

Werengani mutu wathunthu Aroma 13