Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 12:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Patsani zosowa oyera mtima; cerezani aulendo.

14. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere.

15. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.

16. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

17. Musabwezere munthu ali yense coipa cosinthana ndi coipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.

18. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.

19. Musabwezere coipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.

20. Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a mota pamutu pace.

21. Musagonje kwa coipa, koma ndi cabwino genietsani coipa.

Werengani mutu wathunthu Aroma 12