Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 12:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa, Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

2. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.

3. Pakuti ndi cisomo capatsidwa kwa ine, ndiuza munthu ali yense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga, Mulungu anagawira kwa munthu ali yense muyeso wa cikhulupiriro,

Werengani mutu wathunthu Aroma 12