Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 11:26-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. ndipo cotero Israyeli yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti,Adzaturuka ku Ziyoni Mpulumutsi;Iye adzacotsa zamwano kwa Yakobo:

27. Ndipo ici ndi cipangano canga ndi iwo,Pamene ndidzacotsa macimo ao.

28. Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, cifukwa ca inu; koma kunena za cisankhidwe, z ali okondedwa, cifukwa ca makolo.

29. Pakuti 1 mphatso zace ndi kuitana kwace kwa Mulungu sizilapika.

30. Pakuti 2 monga inunso kale simunamvera Mulungu, koma tsopano mwalandira cifundo mwa kusamvera kwao,

31. coteronso iwo sanamvera tsopano, kuti iwonso akalandire cifundo, cifukwa ca cifundo ca kwa inu.

32. Pakuti 3 Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akacitire onse cifundo.

33. Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace kwa Mulungu! 4 Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka!

34. Pakuti 5 anadziwitsa ndani mtima wace wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wace ndani?

35. Ndipo 6 anayamba ndani kumpatsa iye, ndipo adzambwezeranso?

36. Cifukwa 7 zinthu zonse zicokera kwa iye, zicitika mwa iye, ndi kufikira kwa iye. 8 K wa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

Werengani mutu wathunthu Aroma 11