Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 11:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace ndinena, Mulungu anataya anthu ace kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndiri M-israyeli, wa mbeu ya Abrahamu, wa pfuko la Benjamini.

2. Mulungu sanataya anthu ace amene iye anawadziwiratu, Kapena simudziwa kodi cimene lembo linena za Eliya? kuti anaumirira Mulungu poneneza Israyeli, kuti,

3. Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.

4. Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu amunazikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadira Baala.

5. Coteronso nthawi yatsopano ciripo cotsalira monga mwa kusankha kwa cisomo.

6. Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndinchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo.

7. Ndipo ciani tsono? ici cimene Israyeli afunafuna sanacipeza; koma osankhidwawo anacipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;

8. monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.

9. Ndipo Davide akuti,Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa,Ndi monga cokhumudwitsa, ndi cowabwezera cilango;

10. Maso ao adetsedwe, kuti asapenye,Ndipo muweramitse msana wao masiku onse.

Werengani mutu wathunthu Aroma 11