Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 10:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti pakusadziwa cilungamo ca Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa cilungamo ca iwo okha, iwo sanagonja ku cilungamo ca Mulungu.

4. Pakuti Kristu ali cimariziroca lamulo kulinga kucilungamo kwa amene ali yense akhulupira,

5. Pakuti Mose walemba kuti munthu amene acita cilungamo ca m'lamulo, adzakhala naco ndi moyo.

6. Koma cilungamo ca cikhulupiriro citero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? ndiko, kutsitsako Kristu;

7. kapena, Adzatsikira ndani kudzenieko? ndiko, kukweza Kristu kwa akufa.

8. Koma citani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a cikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:

9. kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:

10. pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m'kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso

11. Pakuti lembo litere, Amene ali yense akhulupirira iye, sadzacita manyazi.

Werengani mutu wathunthu Aroma 10