Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 4:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.

10. Aristarko wam'ndende mnzanga akulankhulani inu ndi Marko, msuwani wa Bamaba (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),

11. ndi Yesu, wochedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo anchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine conditonthoza mtima.

12. Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira cifukwa ca inu m'mapemphero ace znasiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'cifuniro conse ca Mulungu.

13. Pakuti ndimcitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo nchito cifukwa ca inu, ndi iwo a m'Laodikaya, ndi iwo a m'Herapoli.

14. Akulankhulani inu Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.

15. Lankhulani abalewo a m'Laodikaya, ndi Numfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.

16. Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikaya, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikaya,

17. Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse.

18. Kulankhula ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukilani zoo mangira zanga, Cisomo cikhale nanu.

Werengani mutu wathunthu Akolose 4