Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 4:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Mau anu akhale m'cisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akarani.

7. Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:

8. amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca ici comwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;

9. pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.

10. Aristarko wam'ndende mnzanga akulankhulani inu ndi Marko, msuwani wa Bamaba (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),

11. ndi Yesu, wochedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo anchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine conditonthoza mtima.

12. Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira cifukwa ca inu m'mapemphero ace znasiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'cifuniro conse ca Mulungu.

13. Pakuti ndimcitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo nchito cifukwa ca inu, ndi iwo a m'Laodikaya, ndi iwo a m'Herapoli.

14. Akulankhulani inu Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.

Werengani mutu wathunthu Akolose 4