Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 3:20-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ici Ambuye akondwera naco.

21. Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.

22. Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;

23. ciri conse mukacicita, gwirani nchito mocokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

24. podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya colowa; mutumikira Ambuye Kristu mwaukapolo.

25. Pakuti iye wakucita cosalungama adzalandiranso cosalungama anaeitaco; ndipo 1 palibe tsankhu.

Werengani mutu wathunthu Akolose 3