Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 2:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndiri nayo cifukwa ca inu, ndi iwowa a m'Laodikaya, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;

2. kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'cikondi, kufikira cuma conse ca cidzalo ca cidziwitso, kuti akazindikire Iwo cinsinsi ca Mulungu, ndiye Kristu,

3. amene zolemera zonseza nzeru ndi cidziwitso zibisika mwa iye.

4. Ici ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.

5. Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.

6. Cifukwa cace monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa iye,

7. ozika mizu ndi omangirika mwa iye, ndi okhazikika m'cikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kucurukitsa ciiyamiko.

8. Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati cuma, mwa kukonda nzeru kwace, ndi cinyengo copanda pace, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu;

9. pakuti mwa iye cikhalira cidzalo ca Umulungu m'thupi,

10. ndipo muli odzazidwa mwa iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

Werengani mutu wathunthu Akolose 2