21. Ndiponso cihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo.
22. Ndipo monga mwa cilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo 2 wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.
23. Pomwepo padafunika kuti 3 zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zeni zeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.
24. Pakuti 4 Kristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, 5 kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu cifukwa ca ife;
25. kosati kuti adzipereke yekha kawiri kawiri; 6 monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika caka ndi caka ndi mwazi wosati wace;